Ezekiel 48:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho kutalika kwa mzindawo kuzungulira ponse kukhale mamita 9,000, ndipo dzina la mzindawo mpaka muyaya likhale ‘Chauta-ali-pano.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pozungulira pake ndipo mikono zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000. “Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala: Yehova Ali Pano.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pozungulira pace ndipo mabango zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi dzina la mudziwo kuyambira tsiku ilo lidzakhala, Yehova ali pomwepo.