Ezekiel 48:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchitana malire ndi Yuda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, padzakhala chigawo chapadera ndithu. Muufupi mwake chikhale makilomita 12 ndi theka. M'litali mwake chikhale ngati zigawo zina, kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Ndipo malo a Nyumba ya Chauta akhale pakati pake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale chopereka muchipereke, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake, ndi m'litali mwake lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi m'malire a Yuda, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo, pakhale copereka a mucipereke, mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace, ndi m'litali mwace lilingane ndi magawo enawo, kuyambira mbali ya kum'mawa kufikira mbali ya kumadzulo; ndi malo opatulika akhale pakati pace.