Ezekiel 5:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu anu chidzafa ndi mliri, kapena chidzaonongeka ndi njala. Chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda. Ndipo chigawo china ndidzachimwazira ku mphepo zonse zinai, pochita kuchipirikitsa ndi lupanga langa losolola.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa ku mphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.