Ezekiel 5:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndimo m'mene udzachitire mkwiyo wanga, ndipo ndidzaŵakalipira mpaka mtima wanga utakhala pansi. Choncho adzadziŵa kuti Ine Chauta ndidalankhula mwansanje pokulangani monga m'mene ndachitiramu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m'changu changa, pokwaniridwa nao ukali wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero mkwiyo wanga udzakwaniridwa, ndipo ndidzakhutitsa ukali wanga pa iwo, ndi kudzitonthoza; ndipo adzadziwa kuti Ine Yehova ndinanena m'cangu canga, pokwaniridwa nao ukali wanga.