Ezekiel 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udzakhala chinthu chonyozeka, ndipo adzakunyodola. Udzakhala ngati chenjezo ndi chinthu choopsa kwa mitundu ya anthu okuzungulira, pamene ndidzakulanga mwamphamvu ndi kugamula mlandu wako mokwiya ndi mwaukali. Ndatero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo chidzakhala chotonza ndi mnyozo, chilangizo ndi chodabwitsa kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikuchitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehova ndanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo cidzakhala cotonza ndi mnyozo, cilangizo ndi codabwiza kwa amitundu akukuzinga, pamene ndikucitira maweruzo mu mkwiyo ndi ukali ndi madzudzulo aukali; Ine Yehovandanena.