Ezekiel 5:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza, kuti ndikuwononge. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuwatumizira Ine mivi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukuthyolerani mchirikizo, ndiwo chakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuwatumizira Ine mibvi yoipa ya njala yakuononga, imene ndidzatumiza kukuonongani, pamenepo ndidzakukuzirani njala, ndi kukutyolerani mcirikizo, ndiwo cakudya.