Ezekiel 5:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiŵiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda mozungulira mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Limodzi la magawo ace atatu utenthe ndi moto pakati pa mudzi pakutha masiku a kuzingidwa mudzi, nutenge gawo lina ndi kukwapula-kwapula ndi lupanga pozungulira pace, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.