Ezekiel 5:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu a ku Yerusalemu adapandukira malamulo anga, kupambana anthu a mitundu ina. Adakhala osamvera kupambana anthu a m'maiko ozungulira. Adakanadi malamulo anga ndipo sadasunge malangizo anga.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa zoposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anakaniza maweruzo anga ndi kucita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendamo.