Ezekiel 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chipongwe chanu nchachikulu kupambana cha anthu a mitundu yokuzungulirani. Simudatsate malamulo anga, simudasunge malangizo anga, koma mudatsata malamulo a anthu a mitundu yokuzungulirani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kuchita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawachita;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza kupokosera kwanu kwaposa kwa amitundu akukuzingani, ndipo simunayenda m'malemba anga, kapena kucita maweruzo anga, ngakhale maweruzo a amitundu akukuzingani simunawacita;