Ezekiel 5:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakulangani ndi chilango chimene sindidakulange nachoni nkale lonse, ndipo sindidzakulanga nachoninso nkutsogolo komwe, poti zolakwa zanu nzonyansa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzachita mwa iwe chimene sindinachichita ndi kale lonse, ndi kusadzachitanso momwemo, chifukwa cha zonyansa zako zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzacita mwa iwe cimene sindinacicita ndi kale lonse, ndi kusadzacitanso momwemo, cifukwa ca zonyansa zako zonse.