Ezekiel 6:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Omba m'manja mwako, ndipo uponde phazi lako pansi kwamphamvu. Tsono unene kuti, ‘Tsokalo!’ chifukwa cha zonyansa zonse zimene banja la Israele lachita. Adzafa ndi nkhondo, njala ndi mliri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, chifukwa cha zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israele; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova Mulungu, Omba manja ako, ponda ndi phazi lako, nuti, Kalanga ine, cifukwa ca zonyansa zoipa zonse za nyumba ya Israyeli; pakuti adzagwa ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri.