Ezekiel 6:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene ali kutali adzafa ndi mliri. Amene ali pafupi adzafa ndi nkhondo. Aliyense wotsala adzafa ndi njala. Ndimo m'mene mkwiyo wanga udzagwere pa iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wokhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene ali kutali adzafa ndi mliri, ndipo amene ali pafupi adzafa pa nkhondo, ndipo amene adzapulumuke ndi kusaphedwa adzafa ndi njala. Kotero ndidzakwaniritsa ukali wanga pa iwo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wokhala kutali adzafa ndi mliri, wakhala pafupi adzagwa ndi lupanga; koma wotsala ndi kuzingidwa adzafa ndi njala; momwemo ndidzawakwaniritsira ukali wanga,