Ezekiel 6:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene mudzaona ophedwa ao ali vuu pakati pa mafano, kuzungulira maguwa ao, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse wogudira, ndi wa thundu uliwonse wa masamba ambiri, ku malo onse kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano ao onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene anthu awo adzagona atafa pakati pa mafano awo mozungulira maguwa awo ansembe, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse watambalala ndi wa thundu uliwonse wamasamba ambiri, kumalo kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano awo onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu ali yense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.