Ezekiel 6:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndidzaŵakantha ndi mkono wanga, ndipo dziko lao lonse ndidzalisandutsa chipululu ku malo ao onse kumene akukhala. Ndidzalisandutsa bwinja kuchokera ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula. Pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa chipululu cha ku Ribula mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndidzawalanga ndi mkono wanga ndi kusandutsa dziko kukhala bwinja. Dziko lonse kumene akukhala kuyambira ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula ndidzalisandutsa bwinja. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzawatambasulira dzanja langa, ndi kulisandutsa dziko bwinja ndi lopasuka, koposa cipululu ca ku Dibla mokhalamo iwo monse; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.