Ezekiel 6:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maguwa anu ansembe adzaonongedwa, ndipo maguwa anu ofukizirapo lubani adzaphwanyidwa. Anthu anu odzapembedza pamenepo ndidzaŵaphera pafupi ndi mafano anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maguwa anu ansembe adzagumulidwa ndipo maguwa anu ofukizira lubani adzaphwanyidwa; ndipo ndidzapha anthu anu pamaso pa mafano anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi maguwa anu a nsembe adzakhala opasuka, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zidzasweka; ndipo ndidzagwetsa ophedwa anu pamaso pa mafano anu.