Ezekiel 6:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono opulumuka mwa inu adzandikumbuka pakati pa anthu a mitundu inayo, kumene adatengedwa ukapolo. Ndidzaŵamvetsa chisoni ndi manyazi chifukwa cha kusakhulupirika kuja ndi kundipandukira kuja, ndiponso chifukwa cha kuika mtima kwao pa mafano. Tsono adzachita nyansi ndi iwo eniakewo poona zoipa zonse zimene adachita, pamodzi ndi zochita zao zonyansa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukira Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wachigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao achigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, chifukwa cha zoipa anazichita m'zonyansa zao zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akupulumuka anu adzandikumbukila Ine kwa amitundu kumene anatengedwa ndende, kuti ndasweka ndi mtima wao wacigololo wolekana ndi Ine, ndi maso ao acigololo akutsata mafano ao; ndipo iwo adzakhala onyansa pamaso pao pa iwo eni, cifukwa ca zoipa anazicita m'zonyansa zao zonse.