Ezekiel 7:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndeu zasanduka chilango cha kuipa kwao. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatsale. Zinthu zao zidzatha, chuma chao chidzathanso, ndipo ulemerero wao womwe udzatha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chiwawa chauka chikhale ndodo ya choipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa chuma chao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chiwawa chasanduka ndodo yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo. Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo. Palibiretu ndipo sipadzapezeka munthu wowalira maliro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ciwawa cauka cikhale ndodo ya coipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa cuma cao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.