Ezekiel 7:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wogulitsa sadzazipezanso pa moyo wake wonse zimene adagulitsa kwa wina, pakuti chilango chidzagwera onsewo, sichingasinthike. Chifukwa cha machimo ake, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti wogulitsa sadzabwera ku chogulitsacho, chinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wake wonse sadzapita pachabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wake m'mphulupulu yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wogulitsa sadzazipezanso zinthu zimene anagulitsa kwa wina chinkana onse awiri akanali ndi moyo, pakuti chilango chidzagwera onsewo ndipo sichingasinthike. Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense amene adzapulumutsa moyo wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti wogulitsa sadzabwera ku cogulitsaco, cinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wace wonse sadzapita pacabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wace m'mphulupulu yace.