Ezekiel 7:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“M'miseu akumenyana, m'nyumba muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Okhala m'mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthengo adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku bwalo kuli kumenyana ndipo mʼkati muli mliri ndi njala. Anthu okhala ku midzi adzafa ndi nkhondo. Iwo okhala ku mizinda adzafa ndi mliri ndi njala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthenso adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.