Ezekiel 7:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati otsala adzapulumukepo, azikakhala ku mapiri, nkumalira ngati nkhunda. Aliyense azidzabuula chifukwa cha tchimo lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, aliyense m'mphulupulu zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene adzapulumuka ndi kumakakhala ku mapiri, azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa. Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, ali yense m'mphulupulu zace.