Ezekiel 7:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kale ankanyada chifukwa cha zodzikongoletsera zao zamakaka. Koma ankazigwiritsa ntchito popanga mafano onyansa. Nchifukwa chake zodzikongoletsera zaozo ndidzazisandutsa zoŵanyansa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina. Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa kukhala zowanyansa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cokometsera cace cokongola anaciyesa codzikuza naco, napanga naco mafanizo ao onyansa, ndi zonyansa zao zina; cifukwa cace ndinapatsa ici cikhale cowadetsa.