Ezekiel 7:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzazipereka kwa anthu akudza kuti azifunkhe. Anthu oipa kwambiri a pa dziko lapansi adzazilanda ndi kuziipitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzachipereka m'dzanja la alendo chikhale cholandika, ndi kwa oipa a m'dziko chikhale chofunkha; ndipo adzachiipsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe. Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda ndi kudziyipitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzacipereka m'dzanja la alendo cikhale colandika, ndi kwa oipa a m'dziko cikhale cofunkha; ndipo adzaciipsa.