Ezekiel 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatuma mitundu ya anthu yoipa kwambiri kuti ilande nyumba zao. Amphamvu pakati panu kunyada kwao kudzaŵathera, pamene ndidzalole mitundu yachilendoyo kuti iwononge malo amene amapembedzerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati cholowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa kuti idzalande nyumba zawo. Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati colowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.