Ezekiel 7:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, padzakhala mphekesera zosatha. Anthu adzafunafuna mneneri kuti aŵalosere zakutsogolo, adzasoŵa ansembe oŵaphunzitsa malamulo, ndipo akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lidzafika tsoka lotsatanatsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatanatsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake, ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake. Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri. Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo, ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lidzafika tsoka lotsatana-tsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatana-tsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.