Ezekiel 7:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idzalira, akalonga ake adzachita mantha. Manja a anthu am'dzikomo adzauma ndi mantha. Ndidzaŵalanga moyenerera machimo ao, ndidzaŵaweruza monga momwe iwowo adaŵeruzira anzao. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzavala chipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera. Ndidzawachitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu idzalira, kalonga adzagwidwa ndi mantha. Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha. Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo, ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzabvala cipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera, Ndidzawacitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.