Ezekiel 7:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano chimalizo chili pa iwe Israele. Mkwiyo wanga ndidzauthira pa iwe. Ndidzagamula mlandu wako potsata mayendedwe ako, ndipo ndidzakulanga chifukwa cha zonyansa zako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimaliziro chili pa iwe tsopano. Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe. Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zanse.