Ezekiel 7:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidzakumverani chifundo kapena kukulekani ai. Ndidzakulangani potsata makhalidwe anu ndiponso chifukwa cha zonyansa zimene mumachita. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, amene ndakulangani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo diso langa silidzalekerera, wosachita chifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine sindidzakumvera chisoni kapena kukuleka. Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako. ‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo diso langa silidzalekerera, wosacita cifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.