Ezekiel 8:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, chaka chachisanu ndi chimodzi cha ukapolo, ndidaali khale m'nyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Mwadzidzidzi mphamvu za Ambuye Chauta zidandifikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chimodzi, mwezi wachisanu ndi chimodzi, tsiku lachisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali caka cacisanu ndi cimodzi, mwezi wacisanu ndi cimodzi, tsiku lacisanu la mweziwo, pokhala ine m'nyumba mwanga, akulu a Yuda omwe analikukhala pamaso panga, dzanja la Yehova Mulungu linandigwera komweko.