Ezekiel 8:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri a Aisraele makumi asanu ndi aŵiri anali ataima pamenepo. Yazaniya, mwana wa Safani, anali pakati pao. Aliyense mwa iwo anali ndi chofukizira lubani m'manja, ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkatuluka m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israele, ndi pakati pao panaima Yazaniya mwana wa Safani, munthu aliyense ndi mbale yake ya zofukiza m'dzanja lake; ndi fungo lake la mtambo wa zonunkhira linakwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamaso pao panaima amuna makumi asanu ndi awiri a akulu a nyumba ya Israyeli, ndi pakati pao panaima Jazaniya mwana wa Safana munthu ali yense ndi mbale yace ya zofukiza m'dzanja lace; ndi pfungo lace la mtambo wa zonunkhira linakwera.