Ezekiel 8:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene akulu a Israele akuchita mumdima muno? Aliyense akupembedza fano lakelake m'nyumbamu. Akunena kuti, ‘Chauta sakutiwona! Chauta walisiya dziko!’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi cocita akulu a nyumba ya lsrayeli mumdima, ali yense m'cipinda cace ca zifanizo? pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko.