Ezekiel 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapita nane ku chipata cha ku Nyumba ya Chauta choyang'ana kumpoto. Kumeneko ndidaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wao wotchedwa Tamuzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anadza nane kuchitseko cha chipata cha nyumba ya Yehova choloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tamuzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anadza nane ku citseko ca cipata ca nyumba ya Yehova coloza kumpoto; ndipo taonani, apo panakhala akazi akulirira Tainuzi.