Ezekiel 8:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adati, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Komabe udzaona zonyansa zina zazikulu kupambana zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Udzaonanso zonyansa zazikulu zoposa izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Waciona ici, wobadwa ndi munthu iwe? udzaonanso zonyansa zazikuru zoposa izi.