Ezekiel 8:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adapita nane ku bwalo lam'kati la Nyumba ya Chauta. Kumeneko, ku khomo loloŵera ku Nyumba ya Chauta, pakati pa khonde ndi guwa, kunali anthu aamuna ngati 25. Adaafulatira Nyumba ya Chautayo, nkhope zao zitaloza chakuvuma, ndipo ankapembedza dzuŵa choyang'ana kuvuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kachisi wa Yehova, pakati pa khonde lake ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kachisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa, napembedza dzuwa kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza nane ku bwalo lam'kati la nyumba ya Yehova, ndipo taonani, pa khomo la Kacisi wa Yehova, pakati pa khonde lace ndi guwa la nsembe, panali amuna ngati makumi awiri mphambu asanu akufulatira, ku Kacisi wa Yehova, ndi kuyang'ana kum'mawa; napembedza dzuwa kum'mawa.