Ezekiel 8:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziwona zimenezi? Ayuda sakukhutira nazo zonyansa akuchita panozi. Koma akufalitsanso zandeu m'dziko lonse. Motero akuutsa ukali wanga, akundipsetsa mtima ndi zochita zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Waciona ici, wobadwa ndi munthu iwe? Cinthu copepuka ici kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti acite zonyansa azicita kunozi? pakuti anadzaza dziko ndi ciwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.