Ezekiel 8:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine ndidzaŵalanga ndili wokwiya. Sindidzaŵayang'ana ndi maso achifundo, ndipo sindidzaŵalekerera. Ngakhale adzalire mofuula kwa Ine, sindidzaŵamvera ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Inenso ndidzachita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawachitira chifundo Ine; ndipo chinkana afuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Inenso ndidzacita mwaukali; diso langa silidzalekerera, osawacitira cifundo Ine; ndipo cinkana apfuula m'makutu mwanga ndi mau akulu, koma sindidzawamvera ine.