Ezekiel 8:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndiyang'ane, ndidaona chinthu chooneka ngati munthu. Munthuyo kuchokera m'chiwunomu kumapita m'munsi anali ngati moto. Kuchokera m'chiwuno kukwera m'mwamba anali ngwee ngati mkuŵa wonyezimira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, chifaniziro cha maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake, moto; ndi kuyambira m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake, monga maonekedwe a cheza, ngati chitsulo chakupsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, cifaniziro ca maonekedwe a moto; kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace, moto; ndi kuyambira m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace, monga maonekedwe a ceza, ngan citsulo cakupsa.