Ezekiel 8:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatambalitsa chinthu chonga dzanja nandigwira tsumba. Pomwepo mzimu wa Mulungu udandikweza mu mlengalenga. Ndipo ngati ndikuwona Mulungu kutulo, udapita nane ku Yerusalemu, nundiika pa khoma loloŵera ku chipata cham'kati choyang'ana kumpoto. Kumeneko kunali fano loputa mkwiyo wa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatambasula conga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati pa dziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku citseko ca cipata ca bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje locititsa nsanje.