Ezekiel 8:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayang'ana kumpoto.” Ine nkuyang'anadi kumpoto. Kumeneko, pafupi ndi guwa pa khomo la chipata, ndidaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako kunjira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga kunjira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa chipata cha guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananena ndi ine, Wobadwa ndi munthu iwe, kweza maso ako ku njira yoloza kumpoto. Ndipo ndinakweza maso anga ku njira yoloza kumpoto, ndipo taonani, kumpoto kwa cipata ca guwa la nsembe fano ili la nsanje polowera pace.