Ezekiel 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuwona zimene Aisraele akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene akuchita kuno, zondichotsa ku Nyumba yanga yoyera? Ndipotu udzaona zonyansa zina zazikulu kuposa zimenezi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzicita? zonyansa zazikulu nyumba ya Israyeli irikuzicita kuno, kuti ndicoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.