Ezekiel 9:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo munthu wovala zabafuta uja, ali ndi zolembera pambali pake, adadzafotokozera Chauta kuti, “Ndachita zimene munandilamula zija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, munthu wovala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake, anabweza mau, ndi kuti, Ndachita monga munandilamulira ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, munthu wobvala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m'cuuno mwace, anabweza mau, ndi kuti, Ndacita monga munandilamulira ine.