Ezekiel 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo ndidaona anthu asanu ndi mmodzi akufika kuchokera ku chipata chakumtunda cha Nyumba ya Mulungu choyang'ana kumpoto chija, aliyense atatenga chida chankhondo. Pagulu paopo panali munthu wina wovala bafuta, atatenga zolembera pambalipa. Onsewo adaloŵa nakaima pambali pa guwa lamkuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya chipata cha kumtunda choloza kumpoto, aliyense ndi chida chake chophera m'dzanja lake; ndi munthu mmodzi pakati pao wovala bafuta, ndi zolembera nazo m'chuuno mwake. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo taonani, anadza amuna asanu ndi mmodzi, odzera njira ya cipata ca kumtunda coloza kumpoto, ali yense ndi cida cace cophera m'dzanja lace; ndi munthu mmodzi pakati pao wobvala bafuta, ndi zolembera nazo m'cuuno mwace. Ndipo analowa, naima m'mphepete mwa guwa la nsembe lamkuwa.