Ezekiel 9:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele udaoneka kuchokera mwa akerubi m'mene unaliri, nufika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Chauta adaitana munthu wovala zabafuta uja amene anali ndi zolembera pambali pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israele unakwera kuchoka pa kerubi, pamene unakhalira kunka kuchiundo cha nyumba, naitana munthu wovala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'chuuno mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unakwera kucoka pakerubi, pamene unakhalira kumka ku ciunda ca nyumba, naitana munthu wobvala bafutayo wokhala ndi zolembera nazo m'cuuno mwace.