Ezekiel 9:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamuuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu, ukaike chizindikiro pamphumi pa anthu onse amene akubuula ndi kulira chifukwa choipidwa ndi zonyansa zimene zikuchitika kumeneko.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova ananena naye, Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe cizindikilo pa mphumi zao za anthu akuusa moyo ndi kulira cifukwa ca zonyansa zonse zicitidwa pakati pace.