Ezekiel 9:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵapheretu onse: okalamba, anyamata, atsikana, tiana, ndi akazi omwe. Koma musakhudze aliyense amene ali ndi chizindikiro chija. Muyambire ku Nyumba yanga yoyera.” Motero iwo aja adayambira kupha akulu a pakhomo pa Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pa malo anga opatulika. Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu ali yense ali naco cizindikilo, ndipo muyambe pa malo anga opatulika, Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.