Ezekiel 9:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ankaŵapha, ine ndidatsala ndekha. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba ndi kufuula kuti, “Aa! Inu Ambuye Chauta, kodi mwakwiya nawo ndithu anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti mudzapha onse otsala ku Israele?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula, ndi kuti, Kalanga ine, Ambuye Mulungu! Kodi mudzaononga otsala onse a Israele pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kupfuula, ndi kuti, Kalanga ine. Ambuye Mulungu! kodi mudzaononga otsala onse a Israyeli pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?