Ezekiel 9:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adayankha kuti, “Uchimo wa Israele ndi Yuda ndi waukulu kwambiri. Dziko ladzaza ndi zophana, mzinda wadzaza ndi zosalungama. Anthu akunena kuti, ‘Chauta walisiya dzikoli. Sakuziwona zimene zikuchitikazi!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mudziwo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israyeli ndi Yuda ndi yaikurukuru ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mudziwo wadzala ndi kukhotetsa mirandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.