Ezra 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono inu nonse amene muli akeake, Mulungu wanuyo akhale nanu. Aliyense mwa inu apite ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda, kuti akamange Nyumba ya Chauta, Mulungu wa Israele. Iyeyo ndiye Mulungu amene amampembedza ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kunka ku Yerusalemu, ndiwo m'Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israele; Iye ndiye Mulungu wokhala m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ali yense mwa inu a anthu ace onse, Mulungu wace akhale naye, akwere kumka ku Yerusalemu, ndiwo m'Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli; Iye ndiye Mulungu wokhala m'Yerusalemu.