Ezra 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho atsogoleri amabanja a fuko la Yuda ndi la Benjamini, ndiponso ansembe ndi Alevi, adayamba kukonzeka, aliyense amene mumtima mwake Mulungu adamupatsa maganizo oti apite kukamanganso Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ananyamuka akulu a nyumba za makolo a Yuda ndi Benjamini, ndi ansembe, ndi Alevi, ndiwo onse amene Mulungu adawautsira mzimu wao akwere kukamanga nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu.