Ezra 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nayenso mfumu Kirusi adatulutsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta zimene Nebukadinezara adaazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu, kudzaziika m'nyumba ya milungu yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kirusi mfumu anatulutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koresi mfumu anaturutsanso zipangizo za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adaziturutsa m'Yerusalemu, ndi kuziika m'nyumba ya milungu yace;