Ezra 1:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kirusi, mfumu ya ku Persiya, idazitulutsa zimenezi nkuzipereka kwa Metiredati, msungachuma wake, amene adaziŵerenga pamaso pa Sesibazara, nduna yaikulu ya ku dziko la Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
zomwezi Kirusi mfumu ya ku Persiya anazitulutsa ndi dzanja la Mitiredati wosunga chumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
zomwezi Koresi mfumu ya ku Perisiya anaziturutsa ndi dzanja la Miteridati wosunga cumayo, naziwerengera Sezibazara kalonga wa Ayuda.